Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 167

Miyambi ya Patsokwe Mutu umodzi susenza denga. -Palibe munthu amene angathe kuchita zonse payekha. Chon- cho, ndi bwino kumadalirana komanso kuthandizana. Mutu wodwala Kasire adatema Kadzidzi. -Zochita za ena zimatha kubweretsera ena mavuto. Si bwino ku- lola kupusitsika ndi maonekedwe. Muvi kalase Nungu. -Munthu ankafuna kulasa Nungu ndipo Nungu inamulasa ndi minga yake. Nthawi zina choipa chimene munthu akufuna ku- chitira mnzake chimatha kumutembenukira. Muvi woyang’anira suchedwa kugwera m’maso. -Mavuto owayang’anira amakula kwambiri, monga matenda. Tisamadikire kuti zinthu zifike poipa. Komanso, kuzengereza kumagwetsera munthu m’mavuto. Muvi woyang’anira suchedwa kulowa m’maso. -Mavuto owayang’anira amakula kwambiri, monga matenda. Tisamadikire kuti zinthu zifike poipa. Komanso, kuzengereza kumagwetsera munthu m’mavuto. Mvera uphungu ndipo utsatire malangizo kuti udzakhale wanzeru m’tsogolo. -Kumvera malangizo kumanthandiza kuti munthu apewe mavuto. Mvula ikakuona litsiro sikata. -Nthawi zina mavuto akakuyamba sakusiya. Mvula ya mpoto kunyenga mkamwini. -Si bwino kutengeka ndi zinthu zomwe zimaoneka ngati si zoipa kwenikweni chifukwa pamapeto pake zimachititsa kuti tidziim- be mlandu kapena tikumane ndi mavuto. 166