Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 166
Miyambi ya Patsokwe
Musamaumirire mtunda wopanda madzi.
-Osamakanirira pa zinthu zomwe zilibe phindu chifukwa zin-
gangotitayira nthawi.
Musamayese ndi masweswe, ndi dazi.
-Mawuwa amenenedwa munthu akamatsimikizira kuti zimene
akunena ndi zoona zenizeni.
Musandiike chibanzi pakamwa.
-Musandiletse kunena zomwe ndikufuna kunena.
Musandiike dzungu pakamwa.
-Musandiletse kunena zomwe ndikufuna kunena.
Musandipatse masamba chifukwa pali kapado.
-Mwambiwu umanena za kukhutira ndi zabwino zimene mun-
thu ali nazo. Ku Africa kuno pamene munthu wadyera nyama
ndiye kuti paterela. Choncho, amafuna kuiwalako kudya
masamba akakhala kuti wapeza nyama.
Musandiyangire nkhata pakamwa.
-Musandiletse kunena zomwe ndikufuna kunena.
Musandiyese chulu cha ndiwo chokwera ndi nthekwe m’chi-
uno.
-Si bwino kuyesa munthu wina ngati wopusa kuti az-
ingokuthandiza nthawi zonse. Tiziyamikira zimene ena amati-
chitira.
Musawongole mbewa yopondaponda.
-Ukadziwa kuti walakwa ndi bwino kungopepesa osachita
makani.
Musayese ndi masweswe, limeneli ndi dazi.
-Si bwino kumanyozera zinthu anthu ena akamanena.
Mutu ukakula sulewa nkhonya.
-Munthu ukakhala wamkulu mavuto onse amafikira kwa iwe.
165