Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 164
Miyambi ya Patsokwe
Munthu salakwira mtengo.
-Kulikonse anthu amalakwirana ndipo palibe amene salakwa.
Choncho, zikachitika ndi bwino tizikhululukirana.
Munthu samenyana ndi maliro.
-Tisamalimbane ndi munthu yemwe ali wofooka kwambiri.
Munthu sangadziteme mphini kumbuyo.
-Timafunika anthu ena kuti atithandize pa zinthu zina.
Munthu satola kanthu ndi chala chimodzi.
-Kugwirizana komanso kuthandizana n’kofunika kwambiri.
Munthu wadyera adanka ndi mvula ya mawawa.
-Munthu wokonda kuchita chiwerewere amafa nsanga potenga
matenda.
Munthu wamagwiragwira samera tsitsi loyera.
-Munthu wamakhalidwe oipa sakalamba.
Munthu waphuma adapsa paphewa.
-Kupupuluma kumawononga zinthu. Ndi bwino kumafatsa.
Munthu wokhulupirika anaipitsira m’basi.
-Nthawi zina kukhala wokhulupirika kwambiri kumabweretsa
mavuto kapena kungachititse kuti munthu achite zochititsa
manyazi.
Munthu wolemera safa ndi chuma.
-Tiyenera kukhala ndi chuma kuti chitithandize pamoyo wathu.
Munthu wongodutsa amene amalowerera mkangano womwe
si wake n’kukwiya nawo, ali ngati munthu wogwira makutu a
galu.
-Osamalowerera nkhani imene sikutikhudza. Munthu amene
wagwira makutu a galu amafunika kusamala chifukwa
akangowasiya makutuwo, galuyo amatha kumuluma.
163