Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 163
Miyambi ya Patsokwe
Mumphasa yongoima mumabisala zoluma zambiri.
-Munthu amene wangokhala chete, timuope.
Mumphuno imodzi simulowa zala ziwiri.
-Umafunika kuchita chinthu chimodzi kaye. Ukaphatikiza zin-
gapo umatha kuwononga zonse.
Mungatero, mwaperekeza mwana wolima.
-Mwambiwu umanenedwa anthu akamadandaula kuti munthu
yemwe amamudalira pamudzi kapena pakhomo wachoka.
Munthu akamafuna kufa, amayamba ndi makutu kutsekeka.
-Kusamvera kumapezetsa munthu mavuto aakulu monga imfa.
Munthu akatsala pang’ono kufa, amayamba ndi makutu kufa.
-Kusamvera kumapezetsa munthu mavuto aakulu monga imfa.
Munthu amene sakhululukira mnzake amakhala akuphwas-
ura mlatho woti aolokerepo yekha.
-Aliyense amalakwitsa, ndiye ngati munthu sakhululukira
anzake, anzakewonso samukhululukira. Ndi bwino mnzathu
akatilakwira tizimukhululukira kuti tsiku lina nafenso tikadzala-
kwitsa adzatikhululukire.
Munthu azilimba ngati mthiko, chipande chilira madzi.
-Tisamangodalira chithandizo chochokera kwa anthu ena ngati
chipande, tizilimba ngati mthiko n’kumadzithandiza tokha.
Munthu ndi Galu, Galu ndi munthu.
-Nthawi zina Galu amachita zabwino kuposa munthu kapenan-
so zabwino zomwe zimafanana ndi zochita za anthu ena. Anthu
ena kuwachitira zabwino sayamika, pomwe Galu ama-
kugwedezera mchira posonyeza kuyamikira.
Munthu sakula pa kamwini, amakula pa kake.
-Munthu aliyense sakhala ndi ulamuliro pa chinthu chamwini
koma chake. Tiyenera kugwira ntchito kuti tipeze zathu.
162