Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 162
Miyambi ya Patsokwe
Mtunkhatunkha udayatsa lipande.
-Munthu ukamakhuthulakhuthula mphale, ina imataika. Nafen-
so tiyenera kukhala anthu okhazikika m’malo momati apa tag-
wira apa tagwira, tikhoza kugwira posagwira kapena kuwonon-
ga zinthu. Lipande ndi mphale.
Mudzi umalimba ndi anyamata.
-Dziko lililonse liyenera kusamalira ndi kunyadira achinyamata
chifukwa ndi amene adzakhale atsogoleri amawa.
Mukanakhala mbewu, tikadangokazinga.
-Mawuwa amanenedwa akamafotokoza za anthu ovuta kapena
ana ovuta. Anthu ena akakwiya amanena mawuwa potanthauza
kuti anthuwo ndi amphulupulu omwe sangawasunge pakhomo.
Mukhoza kusinja chitsiru mumtondo, koma uchitsiru wakewo
sungamuchoke.
-N’zovuta kuthandiza munthu wopusa.
Mulereni ayiwale kwawo.
-Mwana wamasiye kapena wa ena amafunika kumulera bwino
kuti aiwale kwawo kapena mavuto amene akukumana nawo.
Mulimbalimba goli lili m’khosi.
-Munthu ukagwidwa ndi mlandu, ngakhale udziteteze bwanji
zimakhala zopanda phindu chifukwa umboni wonse uma-
kutsutsa.
Mulungu amapatsa wolimbika.
-Tiyenera kumadzithandiza tokha ngati tikufuna kuti Mulungu
atithandize.
Mulungu amapatsa wopirira.
-Tiyenera kumadzithandiza tokha ngati tikufuna kuti Mulungu
atithandize.
161