Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 161
Miyambi ya Patsokwe
Mtima wake waika pa mfuti.
-Kuchita mwano kapena kukula mtima chifukwa choti uli ndi
podalira.
Mtima walasa phaso.
-Mwambiwu umanena za munthu yemwe wakumbukira
kwawo. Ungatanthauzenso kuti ndapeza chokhumba cha mtima
wanga.
Mtima wamnzako ndi m’thumba, sudziwa chomwe chilimo.
-Zomwe wina akuganiza n’zovuta kuzidziwa.
Mtima wamnzako ndi tsidya lina.
-Za mumtima wa munthu wina sungazidziwe.
Mtolo waukulu suchiza njala.
-Ndibwino kumayamikira zimene tili nazo ngakhale zochepa.
Mtsinje umalimba ndi miyala.
-Kudya n’kumene kumathandiza munthu kuti akhale wam-
phamvu.
Mtsinje wa Tinkanena udathera mu Siizi.
-Mawu a akulu amakumbukiridwa pakapita nthawi ndiponso
pamene zomwe amanena zachitikadi. Munthu akakhala wos-
amva akamalangizidwa zotsatira zake amakumana ndi mavuto.
Mtsinje wopanda miyala susunga madzi.
-Miyala ndi imene imathandiza kuti madzi azisungika
mumtsinje. Chimodzimodzinso m’mudzi, mfumu imafuna an-
thu oithandiza pa zinthu zambiri.
Mtsuko sulowa m’chikho, koma chikho ndicho cholowa
mumtsuko.
-Munthu waudindo ndi amene amalandira ulemu kuchokera
kwa otsika, koma iyeyo sapereka ulemu kwa anthuwo.
160