Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 16

Miyambi ya Patsokwe Anyani amaonana zikang’a. -Osamasekana wina akalakwitsa chifukwa nafenso nthawi zina timalakwitsa ngati iyeyo. Mmalo mwake tizikhululukirana ndi kulemekezana. Komanso si bwino kumanyoza kapena kuseka ena pa zinthu zomwe nawenso umachita. Anyani kuseweretsa magwafa. -Mawuwa amanenedwa munthu akamachita chibwana ndi zin- thu zofunika kapena akamaseweretsa zinthu zofunika. Anyani sasekana zikundu. -Osamasekana wina akalakwitsa chifukwa nafenso nthawi zina timalakwitsa ngati iyeyo. Mmalo mwake tizikhululukirana ndi kulemekezana. Komanso si bwino kumanyoza kapena kuseka ena pa zinthu zomwe nawenso umachita. Aonenji adagwira kanthu mumdima. -Anthu onyozeka amatha kuchita zinthu zomwe anthu odziwika sangakwanitse monga kukhala olemera komanso kukhala ndi banja labwino. Aonenji anapha mvuu m’mono. -Anthu ena amaoneka ngati onyozeka mwina chifukwa cha kusauka ndipo ena sawathandiza poganizira kuti palibe chom- we angadzawabwezere. Tsiku lina anthu otere amadzachita chinthu chodabwitsa kapenanso kukhala ndi china chofunika. Kuyeserera n’kofunika kusiyana ndi kungoyang’ana zinthu poganiza kuti sizingatheke. Tisamapeputse nzeru za ena mpaka titaona zotsatira zake. Aonenji anapha njovu ndi mwala. -Anthu ena amaoneka ngati onyozeka mwina chifukwa cha kusauka ndipo ena sawathandiza poganizira kuti palibe chom- we angadzawabwezere. Tsiku lina anthu otere amadzachita chinthu chodabwitsa kapenanso kukhala ndi china chofunika. 15