Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 159
Miyambi ya Patsokwe
Msuma sudyera pomwepo.
-Msuma ndi chakudya kapena zinthu zomwe tapatsidwa
popemphetsa panthawi ya njala. Ndi bwino kukumbukira banja
lako chifukwa nawonso akufuna kudya. Tiziganizira anzathu
ovutika.
Mtakataka kunsengwa, kumunda kumlaka.
-Pali anthu ena omwe amajijirika pakakhala zakudya, kun-
sengwa basi (kale anthu ankapakulira chakudya munsegwa,
mbale zisanabwere). Koma akauzidwa kuti akalime amakana.
Mtanga umakoma ndi kusomekera.
-Pochita zinthu pamafunika kuchita khama kuti zimene tikufuna
zitheke kaya ndi kusukulu kapena pantchito.
Mtaya makoko saiwala, amaiwala ndi m’dya nyemba.
-Munthu ukakhala pamavuto suiwala wina akakuchitira zoipa,
koma wochita zoipazo amaiwala.
Mtedza woola umalavulitsa zonse.
-Kulakwa kwa munthu m’modzi kumaipitsa mbiri ya banja
lonse kapenanso dziko.
Mtengo suphuka masamba usanagwetse akale.
-Kusintha kwenikweni kumabwera ngati munthu wasiya zimene
amachita poyamba.
Mtengo umagwera kumene waweramira.
-Nthawi zambiri ana amachita zimene amaona makolo awo aku-
chita. Ungatanthauzenso kuti munthu akakhala wakhalidwe
loipa amadzafa ndi khalidwe lakelo. N’kovuta munthu kuleka
chizolowezi chake.
Mtengo usamakome pokwera pokha.
-Si bwino kumakonda anthu tikamafuna chinachake kuchokera
158