Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 158
Miyambi ya Patsokwe
Mseka pamwamba, m’kati mwa mtima muli zina.
-Kuonetsa chisangalalo pamaso koma mumtima muli chiwem-
bu.
Msika ndi wekha.
-Kuti zikuyendere umafunika kuchita khama.
Msipu suyenda, imayenda ndi nyama.
-Ngati munthu akusowa chinthu ayenera kupita kukachifunafu-
na chifukwa sichingamupeze pamene wakhalapo.
Msipu wamera m’khola.
-Kuchita mwayi kuti zimene umafuna zachitika mmene umafu-
nira. Kupeza mwayi waukulu.
Msipu wobiriwira udapha mbuzi.
-Mbuzi itapeza msipu wobiriwira inkangodyabe mpaka ina-
phulika mimba. Tisamakomedwe ndi zinthu ngakhale zitakhala
zokoma bwanji chifukwa pamapeto pake tikhoza kupeza
mavuto.
Msirikali wa atate (imfa) ndiye amachotsa chimwemwe.
-Imfa ikamachitika kawirikawiri pakhomo anthu sakhala osan-
galala.
Msonjosonjo andautsa amene ali chete.
-Msonjosonjo ndi kulozana zala. Nthawi zambiri anthu aka-
maloza anzawo chala amapangitsa kuti amene anali chete
akwiye. Ungatanthauzenso kuti nthawi zina anthu apachibale
akamadana zimapangitsa kuti anthu adera alowererepo.
Msonkhasonkha unang’amba thumba.
-Munthu akamangotolera pang’onopang’ono osasiya, zima-
chuluka kwambiri ndipo kenako zmawonongeka. Nthawi zina
ndi bwino kuchita zinthu mosathamanga komanso ndi bwino
kulimbikira kuti zomwe ukufuna zitheke.
157