Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 157
Miyambi ya Patsokwe
ndi akuluakulu. Zikakuvuta anthu omwewa ndi amene amaku-
thandiza.
Mphwayi ndi tsoka, ulesi ndi minyama.
-Munthu wamphwayi sangapeze zimene akufuna. Tizichita kha-
ma pazinthu.
Mphwayi ndi tsoka.
-Munthu wamphwayi kapena waulesi satukuka ndipo ama-
kumana ndi mavuto adzaoneni.
Mphwayi zilibe mtolo.
-Ulesi umabweretsa umphawi. Tiyenera kumagwira ntchito kuti
tipeze zimene tikufuna.
Mpingu saloza ndi chala.
-Mpingu ndi munthu amene amakhala ndi ulamuliro wovo-
mereza zinthu zofunika. Ngati utamuloza ndi chala ndi mwano.
Mwambiwu umatanthazua kuti si bwino kumanyoza anthu om-
we angatithandize.
Mpotepote m’poyamba, potsiriza n’chingwe.
-Zinthu zimaoneka zonyozeka poyamba koma zikakula zimatha
kupanga zazikulu. Mwachitsanzo, kuba zinthu zing’onoz-
ing’ono kukhoza kudzatibweretsera mavuto aakulu.
Mpsalazingo wamukho wapamwala.
-Mawuwa amanena za munthu amene amakhala wochenjera
kwambiri pozemba ntchito kapena mlandu chifukwa chodziwa
kuyankhula.
Mseche udaombola mbiya.
-Aliyense ndi wofunika pambali inayake. Ngakhale ena
azioneka onyozeka tiyenera kumawalemekeza chifukwa akhoza
kudzatithandiza.
156