Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 155
Miyambi ya Patsokwe
n’kupita kukazikhuthura kwina. Amachitanso chimodzimodzi
ndi zimene wamva kumeneko.
Mphamba ikasowa Nkhukhu imatola udzu.
-Ukakhala pamavuto susankha, kunyada umakusiya kaye apo,
n’kuyesetsa kuchita chilichonse kuti uthandizike.
Mphamvu za Ng’ona zili kumchira.
-Anthu audindo amakhala ndi mphamvu chifukwa cha anthu
omwe akuwalamulira. Choncho, ayenera kumalemekeza an-
thuwo.
Mphamvu zimaphetsa.
-Kudzitukumula kumabweretsa mavuto. Ukakhala ndi
mphamvu kumalemekeza ena chifukwa tsiku lina ungadza-
kumane ndi wina wamphamvu kuposa iweyo n’kukumenya.
Mphawi dziko alidyera ku uchi.
-Ngakhale munthu wosauka, anthu ena amamuitana kuphwan-
do ndipo amadya nawo zabwino. Kuthandizana n’kofunika.
Mphawi nayenso ndi mzimu, musamunyoze.
-Munthu aliyense ayenera kulemekezedwa ngakhale wosauka.
Mphechepeche mwa Njovu sapitamo kawiri.
-Ngati tapulumuka pa zoopsa, monga kwa Ng’ona padziwe, si
chanzeru kubwereranso chifukwa mapeto ake tikhoza kugwid-
wa n’kulephera kudzipulumutsa.
Mphemvu m’dyera kum’thiko.
-Mawuwa amanena za munthu wosauka yemwe amapeza zin-
thu movutikira monga chakudya ndi zina.
Mphenzi siimenya mtengo kawiri.
-Pali zinthu zina zomwe zimachitika kamodzi kokha pamoyo wa
munthu. Choncho ndi bwino kumagwiritsa ntchito mwayi
umene tapeza.
154