Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 154

Miyambi ya Patsokwe Mpandamachokero, anakodzera moto wa ana. -Kumakhala ndi chifukwa chenicheni pochoka pamalo monga kuchikamwini kapena pantchito. Osamagwiritsa ntchito zifukwa zosamveka. Mpandamachokero, mkamwini anachokera mamina. -Kumakhala ndi chifukwa chenicheni pochoka pamalo monga kuchikamwini kapena pantchito. Osamagwiritsa ntchito zifukwa zosamveka. Mpani wa mbewa utsatira mwini. -Munthu aliyense amalimbikira kuchita zinthu zake. Amaonet- setsa kuti zachitika bwino kwambiri koposa mmene akanachitira za ena. Ungatanthauzenso kuti choipa chimatsata mwini. Uka- palamula, ngakhale utathawa kapena patapita nthawi yaitali bwanji, tchimo wachitalo limakulondola, ndipo kenako limaku- luma. Mpatse fupa mwana atonthole. -Nthawi zina ndi bwino kumalolera kuti ana achite zofuna zawo. Ndi bwino kumaloleza maganizo kapena zimene anthu ena akufuna kuti aphunzirepo kathu. Mpatseni tione chakhalitsa galu pakhomo. -Pamudzi pakakhala mapokoso kapena mavuto ena, timafunika kuonetsetsa kuti tidziwe chimene chayambitsa vutolo. Mpeni ulibe bwenzi. -Munthu akakhala woipa sakhala ndi bwenzi ndipo anthu ama- muopa kuti tsiku lina angadzawachitire zachipongwe. Mpeni umatha kupha ngakhale mwini wa mpeniwo. Mpeni wakuthwa konsekonse. -Munthu wokonda kukometsa kuwiri, mthirakuwiri. Munthu wotereyu amati akapita uku, amakatapa nkhani kumeneko 153