Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 153
Miyambi ya Patsokwe
Moyo kunyenga.
-Munthu ukakhala ndi thanzi labwino umakhumba utachita
zambirimbiri komanso umatha kunyoza abale ako kuiwala kuti
tsiku lina udzadwala.
Moyo ndi mpamba, usamalireni.
-Kuti munthu achite chilichonse amafunika kukhala ndi moyo.
Moyo saika pachiswe.
-Tiyenera kupewa kuchita zinthu zomwe zingaike moyo wathu
pangozi.
Moyo samanga ndi njerwa.
-Mwambi wosonyeza kuti umafunika kudya kuti ukhale ndi
thanzi.
Moyo uli ngati anyezi, timausenda tikulira.
-Moyo ndi wovuta kwambiri. Masiku ambiri amatha munthu
akuvutika.
Moyo uli ngati moto, umafunika kusonkhezera.
-Kuti zikuyendere umafunika kumasamalira moyo wako.
Moyo wanga ndi kambiya, ndisunga ndekha.
-Palibe munthu angakusamalire moyo wako koposa mwini
wakewe.
Moyo wanga ndi mbiya, ndisunga ndekha.
-Munthu aliyense amasamalira moyo wake, choncho zikakuvuta
suyenera kuloza munthu wina chala chifukwa udindo wosankha
zochita pamoyo wako ulinso m’manja mwako.
Moyo wathombozi wouma kumodzi.
-Thombozi ndi mtengo womwe umauma mbali imodzi n’kukha-
la moyo mbali imodzi koma suferatu. Mawuwa amatanthauza
kuti ngakhale tili moyo, koma tikukumana ndi mavuto ambiri.
152