Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 152
Miyambi ya Patsokwe
Mnzako ali pomwe (mnzako akakhala pafupi).
-Mwambiwu umanena za munthu amene amaoneka ngati mnza-
ko akakhala pafupi, koma akangokhala kumbali amayamba ku-
kunena miseche.
Mnzako si amene umadya naye n’kukhuta, koma amene amati
zikavuta amabwera n’kudzakuthandiza.
-Mnzako weniweni amaonekera pamavuto.
Monga mphuno, maso amatakataka.
-Tisamachite zinthu modzionetsera. Osamasonyeza anthu kuti
ifeyo ndiye abwino kwambiri kuposa ena.
Moto umapita kwatsala tchire.
-Zikagwera ena, dziwa kuti watsala ndi iwe. Ndi bwino ku-
mathandizana kuti nawenso zikakuvuta adzakugwire mkono.
Moto wapathupi sakuuza ndi mnzako.
-Vuto limene ukukumana nalo umalidziwa wekha, suchita
kudikira kuti ena akuuze.
Moto wopanda masekera umavuta kuyaka.
-N’kovuta kuweruza mlandu popanda mboni.
Mowa m’chimera.
-Pochita zinthu pamafunika luso logwiritsa ntchito zinthu zo-
funika kuti zinthu ziyende bwino.
Mowa n’kumwera pamodzi.
-Kuchitira zinthu limodzi n’kumene kungachititse kuti anthu
asangalale kwambiri.
Mowa n’kumwerana.
-Kuti chibale chilimbe pamafunika kuyenderana komanso
kuthandizana.
151