Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 150

Miyambi ya Patsokwe Ananyamula nsima ndi kuika pamphika wa nyama uja kenako n’kuika mphika wa nyama ndi nsima ija pakamwa pa mtsuko umene munali matsukwa uja. Tsoka ndi ilo nyama ndi nsima ija zinagwera m’matsukwa muja. Atatuluka panja kuti akumane ndi mlendo uja, mlendoyo anamuuza kuti, “Pepani ndi wosa- khalitsa, ndimafuna mundigawireko madzi akumwa.” Mlendoyo atamwa madziwo ananyamuka n’kumapita. Mlendo ndi mame, sakhalitsa. -Tisamadane ndi alendo kapena kumawachitira umbombo, chifukwa sachedwa kubwerera kwawo. Mlendo ndi Nkhuku yoyera. -Mlendo amafunika kusamalidwa bwino. Mlendo ndi nkhungu, sachedwa kupita. -Tizilandira bwino alendo chifukwa sachedwa kupita. Mlendo ndiye amapha njoka. -Mlendo ndi amene amathandiza pamavuto ena kapena kupere- ka mfundo yothandiza kwambiri. Mlendo sathyola mphasa. -Alendo sawononga zinthu zambiri, choncho tisamachite man- tha kulandira alendo. Sangamalize mphasa yathu pongogonera usiku umodzi wokha. Mlenje wa misampha amafa ndi msampha. -Munthu amene amachita zoipa zinazake monga kuba, amadzafa ndi khalidwe lomwelo. Mlirira kwawo andanka ndi madzi. -Kuthamanga sikufika. Tisamathamangire kuchita zimene tikufuna chifukwa mapeto ake tikhoza kukumana ndi mavuto. Mlomo wakumwamba ndi wakunsi, pho! -Mwambiwu umanenedwa pamene munthu wapandikizidwa 149