Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 149
Miyambi ya Patsokwe
Mleleni bwino aiwale kwawo.
-Pakhomo pakakhala akamwini kapena alendo timafunika ku-
wasamalira bwino kuti asamadandaule n’kukumbukira kwawo.
Mleme anangowola, sanaike maliro.
-Mleme umakhala ngati zinthu ziwiri, khoswe komanso
mbalame. Mleme utadwala unapita kwa mbalame ndipo zinaka-
na kumulandira. Kenako unapita kwa makoswe ndipo nawonso
anamukana. Mlemewo utafa palibe anaika maliro ake moti
anangowolera pamtunda. Munthu wopanda anzake enieni
amasowa omuthandiza.
Mlendo ndi amene amadza ndi kalumo kakuthwa.
-Mpofunika kumamva maganizo a alendo chifukwa mfundo
zawo zikhoza kukhala zothandiza kwambiri. Mlendo akhoza
kuthandiza pa vuto limene eni mudzi ali nalo.
Mlendo ndi mame, sachedwa kulakatika.
-Tisamachite nkhanza ndi alendo chifukwa sakhalitsa. Komanso
umbombo umaonongetsa zambiri. Nkhani yake imanena kuti,
kalekale panali mayi wina dzina lake Nasiketi. Nasiketi anali
kudziwika kwambiri chifukwa cha umbombo. Tsiku lina
anavuula mphale, ndipo atasinja ufa anaganiza kuti ndiwo
zimene adyere nsima tsikulo zikhale nyama. Anasinjadi ufa
wosalala bwino ndiponso anapezadi nyama yonona bwino
imene anakagula pamudzi woyandikana ndi mudzi wawo. Pa
nthawiyi Nasiketi anali asanataye matsukwa a mphale ija.
Akumaliza kuphika nsima anamva panja munthu wina akuodi-
ra. Poonetsetsa anaona kuti ndi mlendo amene sanali ku-
muyembekezera. Apa nzeru zinamuthera Nasiketi.
148