Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 148
Miyambi ya Patsokwe
Mkwita umodzi sulira m’mwendo.
-Mkwita ndi chibangiri cha m’mwendo. Chikakhala chokha
sichimalira. Zinthu zimayenda bwino kwambiri pakakhala an-
thu ambiri. Mudzi umatchuka chifukwa cha zochita za anthu
onse.
Mlamumwako ndi Likongwe, akalowa mphanga koma ku-
mutsekera ndi masamba.
-Ukamuthandiza mnzako amene ali pamavuto ndiye kuti
wamutsekera ndi masamba. Koma ukakana kumuthandiza
ndiye kuti wamutsekera ndi mwala. Ena akatilakwira tiz-
iwakhululukira.
Mlandu sagula ndi chipanda cha mowa.
-Si bwino kuweruza mlandu mokondera chifukwa choti wina
watipatsa ziphuphu.
Mlandu sugwera pamtengo.
-Kulikonse anthu amalakwirana ndipo palibe amene salakwa.
Choncho zikachitika ndi bwino tizikhululukirana.
Mlandu suwola.
-Ngakhale munthu atathawira kutali, mlandu wake amadzau-
peza patapita zaka zambiri. Munthu akapalamula amakumana
ndi zotsatira za zimene wachita kaya afune asafune.
Mlandu uli m’kamwa.
-Kuyankhula mosasamala kukhoza kutibweretsera mavuto.
Mpofunika kumayamba taganiza kaye tisanayankhule. Tisakha-
le a zikachitika mumvera kwa ife.
Mlatho wathyoka, tsopano tiwoloka bwanji?
-Mawuwa amatanthauza kuti gwero la chithandizo chathu
laphwera, ndiye tikhala moyo bwanji?
147