Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 145

Miyambi ya Patsokwe Mitima sifanana. -Zimene mnzako akuganiza sungazidziwe. Mawuwa amanenedwa anthu akamakayikira zochita za anzawo. Mwachitsanzo, munthu angafunse mwana wake kuti, “Kodi walowetsa chimanga chija?” Mwanayo n’kuyankha kuti, “Ayi, sindinalowetse.” Munthuyo angauze mwanayo kuti, “Kalowetse, mitima sifanana.” Mivi sumaponya yonse. -Poyankhula osamaneneratu zonse chifukwa kusanenako ku- khoza kudzakupulumutsa m’tsogolo. Mjedo umalinda mwini. -Anthu akamanena za ena amafunika kusamala chifukwa akho- za kuwapezerera n’kumva zonse. Mkamwini asamakule mwendo. -Mkamwini ayenera kukhala wofatsa pamudzi m’malo momavuta kapena kulamulira ena. Mkamwini mnzako mpachulu, mtengeze uta. -Ndi bwino kumathandizana mnzathu zikamugwera, chifukwa mwina mawa zidzagwera ife. Ndiye ndi bwino kumathandi- zana. Mkamwini ndi Mlamba, sachedwa kuterereka. -Akamwini komanso anthu ena ofunika pantchito tiyenera ku- wasamala chifukwa tikawachitira nkhanza amachoka n’kutisiya tikuvutika. Mkamwini sadya gaga, likadza dzinja mpatse. -Ngakhale munthu wodyada akavutika, muthandize mosa- yang’ana za kunyada kwakeko. Mkamwini sawiringula. -Ngakhale mkamwini aziona zovuta pakhomo sayankhula. 144