Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 144
Miyambi ya Patsokwe
zimene sizinachitike.
Mimba njosadzitamira.
-Si bwino kumadzitama chifukwa cha zinthu zomwe sizinachi-
tike. Mwachitsanzo, mayi akakhala ndi pakati, sayenera kud-
zitama mpaka atabereka.
Mimba simapha namwino.
-Namwino amangothandiza munthu kuti abereke. Ngakhale
zitavuta bwanji, sangafe chifukwa cha mimba ya munthu wina.
Amangofunika kuthandiza munthuyo basi. Chimodzimodzi
pamlandu, ngati tafunsidwa, tiyenera kusachita mantha po-
longosola zimene tikudziwa chifukwa mimba si yathu.
Minga ikabaya, zula.
-Ukakumana ndi mavuto ndi bwino kupeza njira yothetsera
mavutowo.
Minga ya pansana amakuzula ndi mnzako.
-Pali zinthu zina zomwe sitingakwanitse tokha. Timafunika
kuthandizidwa ndi ena.
Miphika yaphulana.
-Nthawi zambiri anthu okondana amadziwa zimene mnzawo
akusowa. Kuthandizana n’kofunika.
Misala si chamba chokha.
-Pali zinthu zambiri zimene zingachititse kuti munthu akhale
mwanjira inayake. Mwachitsanzo, munthu akhoza kudwala
misala chifukwa cha matenda osati kusuta chamba.
Miseche ilinda mwini.
-Anthu akamanena za ena amafunika kusamala chifukwa akho-
za kuwapezerera n’kumva zonse.
Mitengo yoyandikana imaperesana.
-Anthu akakhala pamodzi salephera kuyambana.
143