Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 143
Miyambi ya Patsokwe
umakumana ndi mavuto ndi iweyo.
Mfumu ndi nkhuti.
-Munthu wamkulu kapena mfumu imadziwa zinthu zambiri
zomwe sangaziulule wambawamba.
Mfumu sidyera kuwiri.
-Mfumu poweruza nkhani siyenera kukondera. Komanso si
bwino kudikira kuti ena atichitire zabwino chifukwa choti ama-
tidziwa, chifukwa akadzachoka tidzasowa kulowera.
Mfumu sikoma kuwiri.
-Mfumu poweruza nkhani siyenera kukondera. Komanso si
bwino kudikira kuti ena atichitire zabwino chifukwa choti ama-
tidziwa, chifukwa akadzachoka tidzasowa kulowera.
Mfumu yandewu simanga mudzi.
-Atsogoleri olongolola kapena okonda ndewu amapweteketsa
anthu awo. Anthu akaona kuti mtsogoleri wawo ndi woipa ama-
samuka pamudzi ndipo mudzi umapasuka.
Mfuti yolasa woombera.
-Nthawi zina zinthu zako zomwe, monga agalu ndi zina ndi
zimene zimakupweteka.
Mimba imodzi siibala nkhoswe.
-Anthu apachibale ayenera kumakondana, chifukwa pamawa
pamadzabwera zinthu zomwe ungadzafune kuti abale ako aku-
thandize. Kuchulukana n’kofunika.
Mimba ndi mtengakako, phewa ndi mtengakaeni.
-Munthu ukakhala ndi chuma umafunika kumachidya, apo ayi
amadzachichecheta ndi ena.
Mimba ndi yanji?
-Mayi akakhala ndi pathupi sitimadziwa kuti mwana amene
adzabadwe adzakhala wotani. Si bwino kumawerengera zinthu
142