Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 142
Miyambi ya Patsokwe
Mfiti Kuliritsa.
-Munthu amene amalira kwambiri pamaliro ndi amene nthawi
zina amakhala kuti wapha munthuyo.
Mfiti yaikazi kulimba moyo.
-Anthu amene amakhulupirira za ufiti amati mfiti yaikazi ndi
imene siimva chisoni popha munthu.
Mfiti yaikazi kuuma mtima.
-Anthu amene amakhulupirira za ufiti amati mfiti yaikazi ndi
imene siimva chisoni popha munthu.
Mfiti zimadziwana.
-Anthu okonda zofanana kaya zabwino kapena zoipa amadzi-
wana.
Mfulumira adameza nsima yamoto.
-Tisamafulumire kuchita kapena kunena kanthu chifukwa
chotengeka. Chifukwa tsiku lina tikhoza kudzanena kapena ku-
chita chinthu chomwe chingadzatibweretsere mavuto.
Mfulumira anadya gaga.
-Kuchita zinthu mofulumira kwambiri kumapangitsa kuti mun-
thu apeze mavuto kapena awononge zabwino zonse.
Mfulumira sachedwa kugwa m’mbuna.
-Kufulumira kapena kupupuluma kumagwetsera munthu
m’mavuto.
Mfumu n’kudzala.
-Amfumu pamudzi kapena pantchito amakhala ngati kudzala
chifukwa nkhani zonse zimakathera kwa iwo.
Mfumu ndi mbatata, ukaongola wathyola.
-Nthawi zambiri anthu omwe ndi otchuka kapena audindo
waukulu amavuta kuwalangiza. Ukalimbana nawo
141