Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 141
Miyambi ya Patsokwe
zinthu mosamala kuti tisapalamule.
Mchenga woyera unathetsa madondwe.
-Pali zinthu zina zomwe zimaoneka zabwino, koma pambuyo
pake zimabweretsa mavuto aakulu.
Mchepera wa Kalulu, mtima ndi phiri.
-Nthawi zina anthu onyozeka kapena ovutika amakhumba ziku-
luzikulu.
Mdima umasaka.
-Pamene walakwira makolo masana, umatha kuthawa. Koma
kukada umapitanso kwa makolo ako n’kukalangidwa.
Cholakwa sichithawika, nthawi imafika ndipo munthu ama-
landira chilango cha zimene wachita.
Mdima wa dzinja udakwatitsa mkazi wonyansa.
-Zinthu zina zikamachitika zimaoneka ngati tsoka, koma nthawi
zina zimabweretsa mwayi. Mwachitsanzo, mkazi wonyansa
adakwatiwa chifukwa cha mdima wa dzinja.
Mdima wamadzulo umathyola mwendo.
-Tisamayende ndi anthu oipa chifukwa akhoza kutipaka
mavuto.
Mesewera sachedwa kubala ndewu.
-Ukaona kuti macheza kapena masewera akulowera kwina-
kwake koipa, ndi bwino kungochokapo chifukwa nthawi zina
masewera abwinobwino kapena macheza amatha kusintha n’ku-
khala ndewu ya mtima bii.
Meta mpala opanda madzi.
-Mawuwa amatanthauza kuchenjeretsa munthu kotheratu.
Mfiti idzafanso.
-Munthu ngakhale woipa bwanji amafabe.
140