Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 140
Miyambi ya Patsokwe
Mbombo ndi mwala, mtengo umataya mayani.
-Mwala sutaya kanthu. Koma mitengo imataya masamba.
Mwambiwu umanena za munthu womana, yemwe safuna kuga-
wira ena zinthu. Munthu wotero amangokhala ngati mwala.
Mbumba n’kudyetsa.
-Munthu ukakhala ndi ana kapena achibale umafunika ku-
mawasamalira.
Mbumba ndi anthu onse.
-Tiyenera kumasamalira achibale onse mosasankha.
Mbuto ya Kalulu idakula ndi tadzaoneni.
-Mbuto kapena kuti malo okhala Kalulu amakhala aang’ono.
Anthu atabwera kuti adzawaone, inakula chifukwa
chopondaponda. Zinthu zazing’ono zimakula zik-
amanenedwanenedwa chifukwa anthu amawonjezerapo bodza.
Mbuzi ikacheuka yasiya mwana.
-Tiyenera kumachita zinthu tikakakhala ndi zifukwa zomveka
zochitira zinthuzo monga kujomba kuntchito, kusiya ntchito ko-
manso zina.
Mbuzi ikalawa zamchere sisiya.
-Mbuzi ikalawa zinthu zokoma sisiya, imavuta koopsa.
Chimodzimodzi ndi munthu amene wayamba khalidwe li-
nalake, zimamuvuta kuti asiye. Amakhala ngati walawa zam-
chere.
Mbuzi ndi mkota.
-Akuluakulu ndi ofunika pamudzi chifukwa amakhala aona
zambiri pa moyo wawo. Ana amatengera zimene makolo awo
amachita.
Mbuzi ya gudu imafikira kumunsi.
-Khalidwe loipa limachititsa kuti munthu alangidwe. Tizichita
139