Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 14

Miyambi ya Patsokwe makolo ake. Andiitana pakalowa njoka, pakalowa mbewa akumba okha. -Mawuwa amanena za anthu omwe amafuna anzawo akakhala pamavuto, koma akakhala pabwino sagwirika. Anditame anasupula mtembo wa eni ake. -Si bwino kumachita zinthu mojijirika kapena kumadzitama pa zinthu zomwe sukuzidziwa bwino. Angakulande, gwiritsa. -Mawuwa amachenjeza munthu kuti asamale zimene ali nazo. Pali anthu ena omwe amafuna kuti zinthu za anzawo zikhale zawo, choncho m’pofunika kumateteza zinthu zako. Angatero ndi maliro ndithu. -Ngakhale munthu utanyada bwanji, tsiku lina udzakhalabe maliro. Choncho, kunyada kulibe phindu, chachikulu ndi ku- kondana ndi anzathu chifukwa ngakhale tiyerekedwe, ti- dzamwalirabe. Angoni satha onse. -Mawuwa amatanthauza kuti ngakhale zinthu zitavuta bwanji, pamakhalabe ena opulumuka. Mwambiwu unayamba pa nthawi imene Angoni ankamenyana ndi Alomwe. Alomwewo anaphika kalongonda, ndiye Angoni ena ataona kalongondayo ndi njala ndi njala, anangoyamba kudya osadziwa kuti ndi zosasuluka. Ambiri anafa ndipo Angoni anayamba kutchula Alomwe kuti angurudi (kutanthauza akuluakulu pankhondo). Masiku ano pa- malo amene zimenezi zinachitikira pamatchedwa pa Ngurudi. Ngakhale anafa ambiri, Angoni ena anapulumuka. Anthu aluso sadyera mwabwino. -Nthawi zambiri anthu amene amalangiza anzawo sakhala ndi makhalidwe abwino. Zimenezi n’zofanana ndi zimene anthu 13