Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 139
Miyambi ya Patsokwe
anakakubweretsera imfa.
Mbeta silola tsiku limodzi.
-Sungafunsire mbeta n’kukulola koyamba. Tiyenera kukhalabe
opirira ngati tikufuna kupeza zabwino.
Mbewa yamanyazi inafera kuuna.
-Mbewa ina sinafune kutuluka kuuna kuthawa utsi chifukwa
cha manyazi ndipo inafera komweko. Tisamachite manyazi ndi
anthu ena pakakhala zofunikira kuchita.
Mbewa zikachuluka siziika masa.
-Pa ntchito pakachuluka anthu, ntchitoyo siyenda.
Mbewa zikachuluka sizitsekera.
-Anthu akachuluka ntchito siyenda bwino. Aliyense aman-
gosiyira mnzake.
Mbewa zikatha amanona ndi aswiswiri.
-Zinthu zabwino zikatha, zotsikirapo ndi zimene zimakhala zo-
funika.
Mbiri ndi ng’oma.
-Mbiri imafalikira mwansanga kwambiri ngati ng’oma.
Mbiri ya mnzako saimira pachulu.
-Osamayalutsa mnzako ponena zimene amalakwitsa kwa ali-
yense.
Mbiya ikasweka siibwereranso, ndikafa ndafa ndatha.
-Chinthu chikaonongeka chimavuta kuchibwezereretsa, monga
munthu akafa wafa basi.
Mbiya ikasweka siiwumbikanso.
-Zinthu zina zikachitika, zachitika zatha. Sizingabwererenso
ngati kale.
138