Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 136
Miyambi ya Patsokwe
monena kuti mawu achinsinsi kapena mawu ena omwe anthu
amanena kuseri, mwina kujeda munthu.
Mawu amakoma kuti naye mdzakazi azikondwa.
-Mawu okoma amasangalatsa aliyense. Tiyenera kukhala osama-
la ndi zomwe timanena kuti tisakhumudwitse ena.
Mawu mpoyamba, otsiriza m’mang’ombe.
-Ndi bwino munthu kusamala mawu oyamba omwe ukufuna
kuyankhula chifukwa ndi amene anthu omvetsera amaw-
erengera kuti ndi zomwe wanena.
Mawu ndi mphepo, sungawatchere msampha.
-Tifune tisafune mawu ayenera kupita kulikonse.
Mawu ndi ng’oma.
-Tizichenjera ndi zimene timanena chifukwa tikayankhula
sabwerakonso.
Mawu ndi oyamba, otsiriza ndi mang’ombe.
-Pa nkhani, mawu oyamba ndiye amakhala nkhani yeniyeni, ob-
wera pambuyo pake amangokhala mang’ombe.
Mawu ngotsogoza (ndi oyamba).
-Munthu akalephera kunena zoona pamene wafunsidwa ndiye
kuti ndi wolakwa. Tiyenera kumayamba kaye taganiza bwino ti-
sanayankhule.
Mawu okoma anatulutsa Ng’azi kumphako.
-Anthu ena akafuna kuchitira ena zoipa kapena akamafuna ku-
wabera amayankhula zosyasyalika, zokokomeza kuti apusitse
munthuyo. Tiyenera kuchenjera ndi anthu amenewa.
Mawu okoma ndi kamba, oipa ndi ndulu.
-Mawu abwino amabweretsa mtendere, oipa amayambitsa nde-
wu, mikangano komanso nkhondo.
135