Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 133
Miyambi ya Patsokwe
amene sakhutira ndi zimene ali nazo. Maso amangofunabe kuti
aone zina zatsopano.
Maso samangira mpanda.
-Maso akhoza kuona chilichonse, kaya ndi chabwino kapena
choipa. Mawuwa amanenedwa ngati wina akunena kuti waona
zinazake zoipa, ndiye potsutsa winayo amati maso alibe mpan-
da.
Matako saleka kuperesana.
-Pamene pali anthu sipalephera kukangana kapena kusemphana
chichewa.
Matako sangatsogole ngakhale atafunitsitsa bwanji.
-Matako amakhala kumbuyo basi, akhoza kufuna kutsogola ko-
ma kwawo n’kumbuyo. Si bwino kumayesa kuchita zinthu zom-
we sizingatheke.
Matama a Kambuzi.
-Makani opanda ntchito kapena ongofuna pofera.
Matenda amabwera pagalimoto koma amachoka wapansi.
-Matenda amabwera kamodzin’kamodzi koma amachedwa kuti
achoke.
Matenda bisani, maliro tidzamva.
-Munthu sungathe kubisa zimene zikuchitika pamoyo wako
chifukwa tsiku lina zidzamveka. Ndi bwino kuuza ena mavuto
athu kuti atithandize. Osamabisa zinthu zimene
simungakwanitse kuzibisa.
Matukutuku a pida.
-Mawu amenewa amanenedwa kwa anthu omwe ndi opanda
mphamvu koma n’kumachita makani kuti akhoza kulimbana
ndi adzitho.
132