Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 132

Miyambi ya Patsokwe zokongola kwenikweni. Maso apatali mkango ukunga nyani. -Chinthu chikakhala patali sichidziwika bwino. Tiyenera ku- chiyandikira kuti tichione bwinobwino. Maso apatali, phiri limakhala losalala, ukaliyandikira si zig- wembe zake. -Zinthu zina zimangokongola m’maonekedwe pomwe si zokon- gola kwenikweni. Maso ndi madiwa. -Nthawi zambiri timatengeka ndi zinthu zoipa kapena zabwino chifukwa choti taziona. Mwachitsanzo, ena amachita chiwerew- ere chifukwa choti aonera zolaula. Maso ndi msampha. -Nthawi zambiri timatengeka ndi zinthu zoipa kapena zabwino chifukwa choti taziona. Mwachitsanzo, ena amachita chiwerew- ere chifukwa choti aonera zolaula. Maso ngati kapachike. -Umbombo si khalidwe labwino. Mawu okuluwika otanthauza kuti akasunge chakudyacho mpaka alendo atapita. Maso saadya. -Kuona chinthu sindiye kuti uchitenga kapena uchiwononga. Mawuwa amanenedwa munthu akamanena kuti akungofuna kuona sikuti atenga chinthucho. Maso sakhuta. -Maso sakhutitsidwa ndi zimene umaona. Tisalole kuti ati- pusitse. Maso sakhutsa n’kupenya. -Kumangoyang’ana zinazake sikungathandize kuti chitheke ko- ma kugwira ntchito. Mawuwa anganenedwenso kwa munthu 131