Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 131

Miyambi ya Patsokwe kuchita mantha kunenepo. Maso akhuta, m’mimba muli njala. -Zokhumba zimakhala zambiri koma zomwe umapeza zimakha- la zochepa. Maso akutali, nyani anadzipha ndi mpeni. -Tsiku lina nyani anaona mlenje akuika mpeni mthumba. Ndiye nayenso atatola mpeni ndipo ankafunanso kuchita chimodzimodzi koma m’malo mwake anadzibaya pamimba n’kufa. Phunziro lake ndi loti tiziyamba taonetsetsa bwinobwino tisanatengere zochita za ena. Maso ali ndi dumbo (njiru). -Maonekedwe okha sangatiuze zambiri za chinthu. Sitingadziwe khalidwe la munthu pongomuona koma zimadalira kucheza naye n’kumudziwa bwinobwino. Maso alibe kuti uku n’kwa apongozi. -Maso amangoona chilichonse, ndipo nthawi zina amaona zin- thu mwangozi. Mwachitsanzo, akhoza kupezeka kuti mwangozi aonera apongozi. Maso alibe mpanda. -Maso akhoza kuona chilichonse, kaya ndi chabwino kapena choipa. Mawuwa amanenedwa ngati wina akunena kuti waona zinazake zoipa, ndiye potsutsa winayo amati maso alibe mpan- da. Maso amaipitsa, kamwa limakonza. -Choipa m’maonekedwe nthawi zina chimakhala chokoma ukachidya. Kuyang’ana mbali imodzi monga kukongola kuma- pusitsa koma mnzeru komanso zoyankhula. Maso apatali amawongola mtengo. -Zinthu zina zimangokongola m’maonekedwe pomwe si 130