Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 130

Miyambi ya Patsokwe zazikulu kwambiri zimatha kutha. Masiku amatha n’kugona. -Tikamayembekezera chinthu timafunika kuugwira mtima chifukwa masiku sachedwa kutha. Masiku amathera kuchitseko. -Masiku sachedwa kupita. Ukamakumana ndi mavuto ndi bwino kudekha chifukwa masiku amavutowo akatha zinthu zikhoza kukuyendera. Masiku anadya atakumana. -Ngakhale munthu atachita zoipa mwanseri, tsiku lina zimaza- dziwika ndipo amachita manyazi. Masiku ndi ambiri, ubweya wa nyama kuchepa. -Tisamataye mtima nsanga, zabwino zili m’tsogolo. Masiku sakoma onse. -Nthawi zina timakumana ndi mavuto ndipo pena timakumana ndi zabwino. Kukumbukira mfundo imeneyi kungatithandize kuti tisamade nkhawa kwambiri zikativuta. Maso a nyama ngofiira, sachedwa kutembenuka. -Zinthu zimatha kusintha nthawi iliyonse, choncho tikakhala pabwino tizikumbukira kuti zinthu zimatha kusintha nthawi ili- yonse. Maso a usiku anagona ndi wakhate. -Pali zinthu zina zomwe sitingazidziwe, mwachitsanzo chifukwa cha m’dima, munthu wina anagona ndi mzimayi wakhate. Osa- masankha kuchita zinthu usanazimvetse bwinobwino. Maso achule saopsa ovula nyanda. -Tisamaope kuuza ena mavuto amene tikukumana nawo kuti atithandize. Ngati tikudziwa zoonadi pankhani inayake si bwino 129