Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 129
Miyambi ya Patsokwe
Mapundi amaphwanya mpini.
-Olima mwamphamvu kwambiri amatha kuthyola mpini.
Chimodzimodzi munthu wovuta kapena wandewu amakumana
ndi mavuto chifukwa cha zochita zakezo.
Masamba auma.
-Mwambiwu umanenedwa pamene munthu wina waphwanya
pangano.
Masewera anabala mwana.
-Nthawi zina zinthu zangati zongocheza zimatha kubweretsa
mavuto aakulu. Ndiye ukaona kuti zayamba kusokonekera, ndi
bwino kungochoka.
Masewera sakhala paulimbo.
-Osamachita chibwana ndi zinthu zomwe zikhoza kutiika
m’mavuto.
Masiku adalinda tsiku kufula.
-Masiku akachuluka umakumana ndi mavuto ena. Umango-
funika kulimbana nawo basi ndipo zimakuyendera.
Masiku adameta Nkhanga mpala.
-Nkhanga inayembekezera kwa nthawi yaitali kuti pangano loti
ikametetse likwaniritsidwe. Ndi bwino kumasunga pangano
lanthu.
Masiku adatsutsa buthu.
-Munthu akalakwa koma osafuna kuvomereza, nthawi imafika
ndipo zimaululika.
Masiku ali pakamchira kanyama.
-Munthu usamataye mtima kuti zimene ukufuna zidzachitika
kalekale chifukwa masiku sachedwa kutha.
Masiku amaoletsa njovu.
-Nthawi ikamapita, ngakhale zinthu zamphamvu komanso
128