Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 128

Miyambi ya Patsokwe mmene kamba amachitira kumangobweza mutu wake m’chikamba chifukwa cha manyazi. Manyazi ndi mantha, anakwatitsa mkazi wadiso limodzi. -Mnyamata wina anakwatira mkazi wa diso limodzi chifukwa chochita manyazi kumuyang’anitsitsa. Munthu usanafunsire kapena kuchita chinachake chofunika kwambiri, umafunika kufunsa ena komanso kuonetsetsa kuti wakhutira nacho. Manyi akale sanunkha. -Zinthu zakale nthawi zina zimakhala zoti zinkagwira ntchito panthawiyo. Tiyenera kumatsatira zatsopano. Mapanga awiri avumbwitsa. -Kuchita zinthu zingapo nthawi imodzi kumachititsa kuti zonse ziwonongeke. Sungachite zinthu ziwiri nthawi imodzi. Mwam- biwu umanena za munthu amene anapita m’phanga lina n’kukaona kuti kukudontha kenako n’kuganiza zopita kwina. Atafika kumeneko anaona kuti bolanso kujaku. Ananyamukanso ulendo wa koyamba kunja, ndipo ali m’njira ananyowa. Mapenyapenya amapha maso. -Tisamangotengeka ndi zilizonse zimene tikuona chifukwa tikhoza kuona zosaona. Kuyang’anayang’ana zinthu kumabwer- etsa mavuto. Mapesi kumunda alinda moto. -Anthu olimba mtima amafunika kuwasamalira bwino kuti zik- ativuta atithandize. Mapundi amadya n’chika. -Munthu wamphulupulu amalangika chifukwa cha zochita zake. N’chika ndi Swiswiri ndipo anthu a mphulupulu amadya Swiswiri chifukwa chosamva. 127