Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 127
Miyambi ya Patsokwe
ng’onayo chifukwa ikhoza kukuika m’kamwa. Si nzeru kuma-
chitabe zinthu zomwe zingatiike m’mavito.
Mano kunamiza.
-Mawuwa amanena za munthu yemwe amakusekerera koma
mumtima akukufunira zoipa.
Mano saona umphawi.
-Ngakhale munthu akhale wosauka, amafunikabe kudya. Zoti
zithu zikuvuta kupeza, mano alibe nazo ntchito.
Manong’onong’o amapha ubwenzi.
-Miseche ikhoza kulekanitsa mabwenzi apamtima.
Mantha ali n’kuseka, ukali uli ndi maliro.
-Pamene munthu wachita mantha amathawa kuti adzipu-
lumutse. Koma akalimba mtima kuthawira panja amakadyedwa
ndi chilomo.
Mantha anadyetsa n’nombwe.
-Chifukwa cha kuopa zirombo anthu ena amaopa kukasaka nya-
ma ndipo amangodyera zopanda pake ngati masamba a
n’nombwe. Munthu ukamaopa kugwira ntchito yomwe
ingakuthandize umphawi umakukwatira.
Manunkhanunkha amapha mphuno.
-Mawuwa amanenedwa pofuna kukhazika mtima anthu pansi,
kuti asamangozunguzika ndi zilizonse.
Manyazi adapha Lambe.
-Lambe ndi mbewa yomwe sinkafuna kutuluka kunja chifukwa
cha manyazi moti inafa ndi njala. Tisamachite manyazi kuchita
zinthu zofunika.
Manyazi anapha kamba.
-Ukamasowa chinachake umafunika kulimba mtima. Kuchita
mantha kapena manyazi kungachitise kuti tizingovutika ngati
126