Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 126
Miyambi ya Patsokwe
m’malo mongotengeka ndi zimene otsatsa malondawo akunena.
Malunje sadya Sakhwi.
-Tisaope tikafuna chinthu chifukwa cha kuwopsedwa ndi maon-
ekedwe a chinthucho. Si bwino kuopa kunena vuto lathu kuti
anthu atithandize.
Mamveramvera amapasula banja.
-Osamangotengeka ndi zonena za anthu.
Mamveramvera anachotsa zolo paukwati.
-Kumangomvera zonena za anthu kukhoza kutitayitsa mwayi.
Komanso potumiza anthu kuti akatiyimire, tizitumiza okhulupi-
rika kuti nkhani isasokonekere.
Manda a mkonzi sakhala akuya.
-Nthawi zina ngakhale munthu ukhale wabwino chotani
pamudzi anthu sayamika. Munthu wina wokumba manda anka-
thandiza anthu pakachitika maliro. Koma atamwalira anthu
anangokumba moti athane nazo ndipo anangolekera m’maondo.
Manda sakana maliro.
-Manda alibe tsankho, amalandira olemera ndi osauka omwe.
Mankhwala a utsi n’kuthawa.
-Munthu ukafuna kupewa zinazake kapena ngati zinazake
sizikukusangalatsa ndi bwino kungochokapo.
Mankhwala amalimba ndi chizimba.
-Mawuwa amatanthauza kuti mlandu umazengedwa bwino pa-
kakhala mboni kapena umboni wooneka bwino.
Mano a Ng’ona umawaona bwino uli m’kamwa mwa
Ng’onayo.
-Ndi mano ochepa omwe amaonekera pakamwa pa ng’ona.
Kungakhale kupanda nzeru kusuzumira kuti uone mano onse a
125