Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 125
Miyambi ya Patsokwe
zawo n’kusokonekera.
Makondamakonda, Buluzi anakonda khonde.
-Zokonda zimasiyanasiyana, choncho mnzathu akamakonda zi-
nazake, tisamuseke chifukwa zokonda zathunso zikhoza kukha-
la zoseketsa kwa anthu ena.
Makutu achitirana nsanje.
-Sizingatheke kumamvetsera munthu ndi khutu limodzi, linalo
n’kumamvetsera wina. Umafunika kumvetsera m’modzi kaye.
Kuchita zinthu ziwiri sikuthandiza.
Makutu sakhuta ndi kumva, maso sakhuta n’kuona.
-Sitingakwanitse kupeze zonse zimene timaona kapena kumva.
Ndi bwino kumakhala okhutira.
Malawalawa anapha milomo.
-Tiyenera kuchenjera ndi zinthu zomwe timakonda chifukwa
pamapeto pake chikhoza kutiika m’mavuto.
Maliro m’mbale.
-Mawuwa amatanthauza ndiwo za nyama.
Maliro n’kulirana.
-Zovuta zikachitika kapena mavuto akabwera timayenera
kuthandizana.
Malonda ali m’maso.
-Munthu umafunika uyambe kaye waona malonda usanagule.
Malonda amakoma ndi kugulana.
-Zinthu zimayenda bwino anthu akamathandizana.
Malonda amakoma ndi n’kuikira (banyira).
-Wamalonda akamapereka banyira, anthu ogula amamukonda.
Malonda ndi m’maso, pakamwa pamangotenderera.
-Munthu ukamafuna kugula kanthu umafunika uchionetsetse
124