Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 124
Miyambi ya Patsokwe
Makale sapangana adalira m’thumba.
-Pamakhala chinthu choululitsa zobisika kapena zachinsinsi.
Makale sapangana.
-Mawuwa amanenedwa pamene anthu awiri apita kumlandu
asanapangane kapena kugwirizana chokanena.
Makani sawombola munthu.
-Kumva zako zokha kukhoza kuika munthu pamoto. Munthu
amayenera kumamva malangizo a ena. Mwayi umakupeza uli
pabwino kale.
Makasu akalira ndiye kuti alipo awiri.
-Tiyenera kumathandizana ngati tikufuna kuti tichite zakupsa.
Mako ndi mako angachepe mwendo.
-Osamanyoza makolo ngakhale atakhala kuti ndi osaoneka
bwino. Chikondi cha pachibale sichitha.
Mako ndi mako usawaone kuchepa mwendo.
-Osamanyoza makolo ngakhale atakhala kuti ndi osaoneka
bwino. Chikondi cha pachibale sichitha. Tizipereka ulemu kwa
makolo ngakhale ali onyozeka.
Makolo amasamalira ana mano awo akamamera, ana amasa-
malira makolo mano awo akayamba kuguluka.
-Ndi bwino kumasamalira makolo chifukwa nawonso anavutika
kutisamalira tili ana.
Makolo amasamalira ana, mano a anawo akamamera; pomwe
ana amasamalira makolo awo, mano a makolowo akayamba
kuguluka.
-Ana ali ndi udindo wosamalira makolo awo akamakalamba.
Makolo atsoka amati, “ndinadya chiyani ine kuti ndibereke
chitsilu ngati chimenechi?”
-Pali ana ena omwe ngakhale tiwalele bwino, amatha kuyamba
123