Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 123
Miyambi ya Patsokwe
Madzi saiwala khwawa.
-N’kovuta munthu kuleka chizolowezi chake. Si bwino kuiwala
makolo kapena zinthu zina zofunika.
Madzi saiwala mkolokolo.
-Si bwino kuiwala makolo kapena zinthu zina zofunika. Anga-
tanthauzenso kuti zimakhala zovuta kuiwala zimene unazolow-
era.
Mafukufuku sayenda, imayenda ndi nyama.
-Ngati wafunsira mkazi amayembekezera kuti uzimuyendera
kuti adziwe kuti umamukondadi. Munthu akabwereka ngongo-
le umamupitira kwawo chifukwa kawirikwawiri sangabwere
kudzakupatsa ndalama yako.
Mafuta amagwera pa anzake.
-Ulemerero umabwera pamene pali ulemerero kale. Mwayi
umakupeza uli pabwino kale.
Magulugulu a mvula anathawitsa mkamwini kumudzi mvula
isanagwe.
-Si bwino kumataya mtima msanga tikakumana ndi mavuto
kapena tikamva zinazake zokhumudwitsa. Tisamapupulume
kuchita zinthu tisanamvetse bwino nkhani.
Magwiragwira amapha manja.
-Kugwiragwira kumabweretsa mavuto.
Maimvaimva adathawitsa zolo paukwati.
-Mamveramvera amabweretsa zowawa. Ndi bwino kuchita zin-
thu zimene ukuona kuti zikuthandiza m’malo momvera anthu
ena.
Maimvaimva amapha makutu.
-Si bwino kumangokhulupirira zonena za ena tisanafufuze
bwinobwino.
122