Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 122
Miyambi ya Patsokwe
Madzi akataika sawoleka.
-Zinthu zikataika kapena zikasokonekera, zimakhala kuti
zasokonekera basi.
Madzi akatayika sawoleka.
-Pali zinthu zina zomwe zikachitika, sizingathekenso kuzibwe-
zeretsa.
Madzi amachuluka ndi a m’njira.
-Zinthu zazikulu zimayamba pang’onopang’ono, monga mtsinje
umadzadza ndi madzi a m’ngalande.
Madzi amakoma akakhala m’chinkho, koma akakhala
mumtsinje amapha.
-Pali zinthu zina zoopsa zikakhala malo ena kapena zikakhala
zambiri.
Madzi apamwala amatunga ndi amene walawira.
-Ukafuna kuchita chinachake umafunika kuchita zinthu mofu-
lumira. Ulesi umamanitsa zambiri.
Madzi apamwala watunga walawira.
-Ukafuna kuchita chinachake umafunika kuchita zinthu mofu-
lumira. Ulesi umamanitsa zambiri.
Madzi n’kulubza, mchenga upita pansi.
-Mawu onenedwa ndi anthu awiri odziwana kuti amuchenjerere
munthu wina.
Madzi ndi moyo.
-Madzi ndi ofunika kwambiri pa moyo wa munthu.
Madzi odikha ndi amene amalowa pansi.
-Munthu waphee ndi amene amakhala ndi maganizo akuya
kapena oopsa.
Madzi oyera umasambira kumutu, akuda kumapazi.
-Alendo mumawapatsa zabwino, zinazo zimakhala zanu.
121