Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 121
Miyambi ya Patsokwe
M’thunzi umodzi suthera nkhani.
-Ndi bwino kukhala odekha m’malo mopupuluma kuti zinthu
zina zithe mwachangu.
M’tsuko sulowa m’chiko, koma chikho ndicho chimalowa
mumtsuko.
-Munthu waudindo ndi amene amapatsidwa ulemu, koma iyeyo
sachita zimenezo kwa ena omwe ndi otsika.
M’yang’ana dzuwa adasochera.
-Ngati tikukayika kapena sitikudziwa zoyenera kuchita ndi
bwino kufunsa kuti tichite zinthu moyenera.
Mabatani akunsana amakumanga ndi anzako.
-Timafunika kuthandizidwa ndi anthu ena.
Mabingu a mvula anathawitsa mkamwini kumudzi mvula
isanagwe.
-Osamapupuluma kusiya kuchita zinthu chifukwa cha zinthu
zomwe sitikutsimikizira ngati zingachitikedi.
Machokero a pabwalo.
-Munthu akatsanzika kuti akubwera kukatenga chinachake
ndiyeno osabweranso, anzake amanena kuti, “anangonama kuti
akukatenga chinthu, anali machokero a pabwalo.”
Madoli (matodwe) adafera mchenga woyera.
-Zinthu zina zimangokongola m’maonekedwe zili zosathandiza
kwenikweni.
Madoli anafera mchenga woyera.
-Pali zinthu zina zomwe zimaoneka zabwino zomwe pambuyo
pake zikhoza kutiika m’mavuto.
Madzi adzadza, mlamba usangalale.
-Munthu ukapeza zinthu zabwino umafunika kusangalala.
120