Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 120
Miyambi ya Patsokwe
M’mera m’poyamba.
-Ndi bwino kumachita zinthu moyambirira. Ngati ukufuna kuti
ana ako akule bwino, ndi bwino kuyamba kuwalangiza
kuyambira ali aang’ono. Kuti tidzakolole zambiri, timafunika
kudzala moyambirira. Kuchita zinthu moyambirira n’kofunika
kwambiri.
M’mimba ndi m’chipala.
-Ngakhale ana obereka mayi m’modzi amatha kukhala osiyana
m’maonekedwe, makhalidwe komanso zochita zawo. Pa chipala
ndi pamene amasulira zinthu zosiyanasiyana monga makasu,
mipeni, zikwakwa ndi zina.
M’mphechepeche mwa njovu sapitamo kawiri.
-Ngati munthu wapulumuka pa vuto mwamwayi, si bwino
kubwereza kuchitanso zomwezo.
M’mwemo anakhazikitsa tsindwi pakhudu (pambali).
-Munthu waulesi amawononga zinthu ngakhale zake zomwe.
M’nyumba mukasowa ufa, sataya mkute.
-Tisamawononge zinthu zathu ngakhale titakhala pabwino,
chifukwa tikhoza kudzazifuna mawa.
M’nyumba yamwini saotcheramo mbewa.
-Si bwino kumachita chilichonse chomwe timachita kwathu
tikapita kuchilendo chifukwa mwina eni akewo sasangalala
nazo.
M’thengo saikizamo bowa.
-Munthu ukakhala ndi chinthu ndi bwino kuchisamala chifukwa
ukapusa anzako akhoza kukutolera.
M’thumba lamwini sapisamo dzanja.
-Osamayamba zinthu podalira ndalama za m’thumba la munthu
wina.
119