Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 119

Miyambi ya Patsokwe M’bakadya adalinda kwawukwawu. -Kuzengereza kapena kukomedwa pochita zinthu kumabwer- etsa mavuto. M’bakadyam’bakadya adachoka fumbi lili koboo. -Kuumirira zinthu ndi koipa. Osamakomedwa kuchita zinthu zomwe tikudziwa kuti zikhoza kutibweretsera mavuto. M’chenicheni, mpeni wa Chiwoko. -Mpeni wa a Chiwoko ndi mpeni wakuthwa konsekonse. Mwambiwu umanenedwa ngati munthu waweruza mopanda chilungamo mlandu wa m’bale wake. Munthu akaweruza mlan- du wa m’bale wakeyo mokondera amati ndi mpeni wa Chiwoko. M’chiuno mwa mwana simufa Nkhuku. -Mwana ngakhale achite zabwino zotani sayamikiridwa chifu- kwa anthu ena amati mwana sangachite zinthu zopambana. Mwachitsanzo, mwana akhoza kuvina bwino kwambiri, koma anthu sangamufupe Nkhuku. Nthawi zambiri anthu amene amalimbikira ntchito sadyerera, amadyerera ndi mabwana awo. M’dzaonanji adaona Mbawala yake tsiku lamvula. -Munthu wonyozeka amadzapeza mwayi womwe sitinauyembekezere chifukwa choti wachita khama. M’dziko la akhungu, wadiso limodzi amakhala mfumu. -Anthu olongosokako ndi amene amalamulira. M’kamwam’kamwa mudatha lichero la mapira osaviika. -Tisamangofulumira kulonjeza kuti tidzachita chinachake, chifu- kwa tikadzalephera tidzachita manyazi. M’madzi munanyenga Chule. -Mawuwa amanena za munthu amene amadzitukumula chifu- kwa cha maonekedwe kapena kudzisamalira kwake, kumango- funa kukhala wosiyana ndi anzake kumene wapita. 118