Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 116
Miyambi ya Patsokwe
Ladza dzinja, ana anole mano.
-Mavuto akakupanikiza kumakumbukira kuti amatha ndipo chi-
sangalalo chimabwera.
Lakoma thendo, nyama ilowa m’mano.
-Nyama ndi yokoma kwambiri koma kuipa kwake imalowa
m’mano. Munthu akakhala ndi moyo wosalira zambiri savutika.
Lambulire, nawe ndidzakulambulira.
-Zinthu zimayenda mukamathandizana.
Laponda diwa lamphawi.
-Nthawi zina munthu amapeza mwayi womwe sama-
yembekezera.
Lekani! manong’onong’o adadzutsa njovu.
-Zinthu zazing’ono zimatha kuyambitsa zazikulu.
Mwachitsanzo, phokoso laling’ono lingachititse kuti njovu idzu-
ke n’kupha anthu.
Lende n’kukankhana.
-Mnzako akukuchitira zabwino nawenso ndi bwino kumuchitira
zabwino.
Katungwe n’kukankhana.
-Zimakhala bwino kumathandizana.
Lero lomwe lidadetsa Nthengu.
-Nthawi zina ndi bwino kudikira pochita zinthu chifukwa
tikachita mofulumira nthawi zina zinthuzo sizichitika bwino.
Kuchita zinthu modekha kumathandiza kuti zinthu zisasokon-
ekere. Mwachitsanzo, nthengu inkafuna kuti aimalize kuipenta
tsiku lomwelo. Chifukwa chosafuna kubweranso mawa, anai-
paka penti wakuda.
Lero muchira ndi madzi okha.
-Mkuluwikowu umatanthauza kuti pakhomo palibe chakudya.
115