Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 115

Miyambi ya Patsokwe Kwanu sikutalika. -Kwanu kungatalike bwanji, umachita zotheka kuti ukafikeko. Kwapsa kwamera, koma kwatsala thengo. -Zinthu zikachitika sizitheratu, mwachitsanzo mlandu ukhoza kutha koma anthu n’kumasungiranabe chakukhosi. Kwatsala tchire moto umapita komweko. -Chaona mnzako lero mawa chidzaona iwe. Kweza Mbawala m’mwamba. -Osamadziika dala m’mavuto pokhala dala pamalo oipa kapena kuchita zosayenera. 114