Miyambi ya Patsokwe
kulemekeza amene amatisamala ndi chinthu chofunika kwambi-
ri.
Kuzingwa kwa Kalulu kukapsa.
-Anthu ambiri amakhala osangalala ngakhale ndi zochepa zom-
we ali nazo. Koma zimene amadalira monga makolo akamwali-
ra, amakhala m’mavuto aakulu, osowa nawo pothawira.
Kwa amake a mwana ndiko kuli madyera.
-Mwana kapena munthu aliyense amasangalala kwa amayi ake
chifukwa mayi sanganyoze mwana wake.
Kwa ena n’chitsiru, amake ati mwana.
-Makolo amakondabe ana awo ngakhale atakhala ndi mavuto
ena.
Kwa eni kudyetsa nthanga dzungu ukulifuna.
-Munthu ukakhala kwa eni umakhala wopanda ufulu wochika
kapena kuyankhula chilichonse chimene ukufuna. Tiyenera ku-
khala odzichepetsa tikakhala kwa eni.
Kwa eni kuika moyo, kuipira kudwala.
-Ukakhala kwa eni umapulumuka zoipa zochokera kwa abale,
koma ukadwala umakumbukira kwanu.
Kwa eni kulibe “mkuwe,” ukakuwa wadzikuwira nkhondo.
-Munthu ukakhala kwa eni sumalamulira, ukachita zimenezi
amatha kukuthamangitsa.
Kwa eni kulibe mkuwo, mutu wa nkhuku n’chiwalo.
-Ukakhala kwa eni umachita zomwe kwanu sukanachita monga
kudya mutu wa nkhuku pomwe kwanu umadya ziwalo zofewa.
Kwa eni kusunsitsa msuzi ndiwo ukuzifuna.
-Munthu ukakhala kwa eni umalephera kuchita zomwe
ukadachita uli kwanu.
112