Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 111

Miyambi ya Patsokwe kuphunzitsidwa kuyambira ali wam’ng’ono. Kuyandikana si kuyanjana. -Kudziwana si kukhala pamodzi ayi, koma kuyenderana. Kuyasamula n’kupempha, mwana wa mfulu adziwa yekha. -Kuyasamula n’kupempha mosafuna kuonetsera. Choncho, munthu wachifundo amadziwa yekha chochita. Kunyamula mpanda woola n'kuchulukana manja. -Kuchitira zinthu limodzi komanso kuthandizana n'kofunika. Kachepatsonga mtima ukunga phiri. -Munthu wooneka monyozeka koma ali wanzeru komanso wamphamvu kwambiri. Kalowa m’nkhutu kalowa. -Chimene munthu wamva wamva basi. Tizisamala poyankhula. Kuyenda awiri si mantha. -Anthu akakhala awiri amatha kuchita zinthu modalirana ndipo amatha kuthandizana wina akapeza mavuto. Kuyenda awiri si mantha. -Anthu mukakhala pagulu mumathandizana komanso mumalimbitsana mtima. Kuyenda koma pamodzi. -Anthu mukakhala pagulu mumathandizana komanso mumalimbitsana mtima. Kuyenda m’mawa n’kudya nawo. -Munthu akafuna kugwira ntchito yake bwino amafunika ku- lawira. Kuyenda n’kupiringizika. -Paulendo sungadziwe pomwe ukafikire. 110