Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 110
Miyambi ya Patsokwe
Kutsutsa ngomwa n’kuivulira.
-Potsutsa munthu umafunika kukhala ndi umboni weniweni.
Kutukwana samangira mtanda.
-Munthu uyenera kumachita manyazi ukapanga chinthu
cholakwika.
Kuuma kwa mutu kumachititsa kuti pakamwa patsegule
m’mimba.
-Anthu opanda nzeru ndi amene amalongolola kwambiri.
Kuutsa mapiri pachigwa.
-Mawuwa amanenedwa ngati munthu wachititsa kuti anthu
ayambane, kaya ndi apachibale kapena ena adera.
Kuvala khoza ndi kuwolowa dzanja.
-Khoza ndi chibangiri. Kuti munthu avale chibangiri amafunika
kufewetsa dzanja lake. Kuti munthu azikondedwa kapena ku-
patsidwa zinthu amafunika kukhala wopatsa. Komanso munthu
wopatsa sachita kudikira kuti ena amupemphe kuti awathan-
dize.
Kuwerengera madzi a mphutsi.
-Mayi wina amawiritsa madzi kuti aphere mphutsi, koma mlen-
do ankaganiza kuti ndi madzi a nsima. Mawuwa amatanthauza
kuwerengera zinthu zosakhala zenizeni.
Kuwerengera mbewa ndi michira yomwe.
-Kuwerengera ndi zinthu zoti palibe zomwe.
Kuweta Galu ndi kum’ponyera chakudya.
-Mwambiwu umatanthauza kuti kuti munthu akhale ndi ana
kapena anthu ena, amafunika kuwadyetsa komanso kuwasama-
lira.
Kuwongola mtengo mpoyamba.
-Kuti munthu akhale ndi makhalidwe abwino ayenera
109