Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 11

Miyambi ya Patsokwe kwa adani ako monga mmene zinachitikira ndi Yesu. Ana- perekedwa ndi wophunzira wake. Ana a ngoma opanda makutu. -Mawuwa amanenedwa kwa ana osamvera. Amawayerekezera ndi ana a ngoma omwe alibe makutu. Anadya matako a galu. -Si kawirikawiri kuona galu atakhala pansi ndi matako ake. Nthawi zonse amangokhalira kuyendayenda. Ndiye munthu akakhalanso kuti samakhala pansi, amangokhalira kuyendayen- da amati, “anadya matako a galu.” Anadya mtedza wa ching’onga. -Mwambiwu umanena za munthu amene sachedwa kuiwala zin- thu. Ching’onga chimati chikabisa kanthu chimaiwala msanga, ndipo anthu amadzatola. Anadya mtima wa Kalulu, nkona ali ndi mtima wokaluluka. -Mwambiwu umanena za munthu amene ali ndi mtima wap- achala, wosachedwa kupsa mtima. Anadya mtima wa Sontho. -Mwambiwu umanena za munthu amene amachita zinthu mopupuluma kapena mofulumira kwambiri. Sontho ndi mbewa imene imakonda kukhala m’makoko a chimanga chikakhala kuti sichinakololedwe. Ndiyeno mbewayi imasonthoka ikamva pho- koso la anthu okolola. N’chifukwa chake amaitchula kuti Sontho. Choncho, chifukwa chakuti munthu wopupuluma amachita zofanana ndi zimene mbewazi zimachita zikamathawa m’makoko a chimanga, amangoti anadya mtima wa Sontho. Anafa ndi nsanjikizo. -Anthu akamanena za munthu amene wadzigwiritsa chifukwa choti ananena zinthu zambirimbiri kapena ananena zinthu 10