Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 109

Miyambi ya Patsokwe Kuti ndidye ndiponda muno, otsala ngam’kamwa. -Mwambiwu m’Chichewa chamakono umanena za munthu amene akunena kuti, “Kuti ndipeze chakudya ndiponda muno, sindikusamala zomwe anthu atanene chifukwa angokhala am’kamwa.” Tisaleke kuchita zinthu zofunikira poopa manong’onon’go. Anthu sadzaleka kunong’ona akaona wina akuchita zinazake. Kutola fulu ndi kulawira. -Ngati munthu ukufuna kugwira ntchito bwino ndi bwino ku- lawira. Kutola khobwe n’kum’mawa. -Munthu akafuna kuchita chinthu amafunika kuchichita mwan- sanga. Kutola khobwe ndi m’mawa. -Tisamazengereze tikafuna kuchita kanthu. Tisamachedwe pochita zinthu ngati omwe akukolola khobwe, akachedwa khob- we yense amathera pansi n’kuthetheka. Tikafuna kugwira ntchi- to ndi bwino kulawira kapena kuchita moyambirira n’kufunika. Kutola nkhwangwa ndi mpini womwe. -Mawuwa amanenedwa pamene munthu wachita mwayi waukulu kwambiri umene samayembekezera. Kutola si kuba. -Kutola kanthu si kuba, koma ukatenga pakhomo pa munthu osapempha. Kutsutsa Galu n’kukumba. -Ngati munthu akukana kuti sanalakwe pamafunika kukhala mboni yoti imutsutse. Si bwino kutsimikizira chinthu usadapeze umboni wokwanira. 108