Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 108
Miyambi ya Patsokwe
Kutapa nzeru m’thumba la Likongwe.
-Mawuwa amanena za munthu amene amayamba kaye wafunsa
ena asanachite zinthu. Kuchita zimenezi kumathandiza munthu
kuchita zinthu mwanzeru.
Kutaya udzu womwetamweta.
-Mawuwa amatanthauza kutaya mwayi wopezapeza.
Kutchena ndi kupirira.
-Kuti atsikana kapena azimayi atchene, kaya ndi m’mutu, ama-
funika kupirira ululu. Mwachitsanzo, ena amapsa ndi livuloni
koma samasiya.
Kutemetsa nkhwangwa pamwala.
-Kutaya mwayi pogwiritsa ntchito chinthu mosayenera. Mawu-
wa angatanthauzenso kukanitsitsa.
Kutengera zinthu pamgong’o.
-Kutenga zinthu udyo kapena kumva zinthu molakwika. Si
bwino kumazezeduka kapena kumajijirika kwambiri.
Kuthamanga sikufika.
-Kuchita zinthu mofulumira kwambiri kumabweretsa mavuto
kapena kuwonongetsa zinthu.
Kuthawa mtswatswa wako womwe.
-Kunamizira kukana chinthu chomwe wachita ndiwe wemwe.
Kuthawa ndewu si mantha, koma kusamala mano.
-Kupewa zinthu zobweretsa mavuto ndi nzeru kusiyana ndi
kuzichita n’kupeza mavuto.
Kuthyola ndiwo n’kuwerama.
-Munthu akafuna kupeza zinthu amafunika kugwira ntchito
molimbika.
107