Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Miyambi ya Patsokwe | Page 107
Miyambi ya Patsokwe
Kusamala mano si kutsuka mkamwa kokha, komanso kupewa
zigogodo.
-Ndi bwino kumapewa ndewu chifukwa zimabweretsa mavuto.
Kuseri kulinji?
-Ngakhale mafumu amanyozedwa kumbali. Munthu sungadzi-
we zomwe ena amanena kuseri.
Kuseri kumvenji?
-Munthu ukakhala pawekha zambiri zimakupita.
Kuseri kutukwanitsa a Chiwere.
-Ngakhale mafumu amanyozedwa kumbali. Munthu sungadzi-
we zomwe ena amanena kuseri.
Kuseri kwecheche, adagwidwa msanasana.
-Pakhalekhale choipa chilichonse chimene chimachitidwa mseri,
chimadzaonekera poyera.
Kusiya fumbi.
-Limeneli ndi bodza lonenedwa ndi munthu nthawi yamavuto.
Nthawi zinanso angatanthauze kupulumuka pamlandu chifu-
kwa chodziwa kuyankhula mochenjera. Angatanthauzenso
kuthawa ndi liwiro lalikulu.
Kusiya n’kute n’kulinga utatolatola masana.
-Mwambiwu umatanthauza kuti munthu amene amapeza zo-
chepa, sakhala ndi zambiri zosunga.
Kusochera ndiko kuphera kulupsa.
-Akamati munthu wataika ndiye kuti wachita zinthu zomwe
sumafuna kuchita kapena walephera kuchita zomwe amafuna.
Kuswa mtedza chokhala n’kwabwino.
-Kuti ntchito igwirike bwino pamafunika kuifatsira.
106